8 Anthu inu mupereke gawo lina monga chopereka chanu. Gawolo lichite malire ndi gawo la fuko la Yuda ndipo likhale mikono 25,000 m’lifupi.+ M’litali mwake lifanane ndi magawo a mafuko aja. Malire a gawolo ayambire kum’mawa kukafika kumadzulo. Malo opatulika akhale pakati pa gawo limeneli.+