-
Ezekieli 48:21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 “Malo otsala a mbali iyi ndi mbali inayo ya chopereka chopatulika ndiponso ya mzinda+ akhale a mtsogoleri+ wa anthu. Kumbali ya kum’mawa, malowo achite malire ndi malo operekedwa aja ndipo akhale mikono 25,000 m’lifupi. Kumbali ya kumadzulo, malowo achite malire ndi malo operekedwa aja ndipo akhale mikono 25,000 m’lifupi. Malo a mtsogoleriwo achokere kumbali ya kum’mawa kukafika kumbali ya kumadzulo mofanana ndi magawo a mafuko aja.+ Malo omwe ndi chopereka chopatulika komanso malo opatulika a Nyumba ija akhale pakati pa malo a mtsogoleriwa.
-