-
Ezekieli 9:2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Ndiyeno ndinaona amuna 6 akubwera kuchokera kuchipata chakumtunda+ choyang’ana kumpoto, aliyense atanyamula chida chake chophwanyira. Pakati pawo panali munthu mmodzi atavala zovala zansalu.+ M’chiuno mwake munali kachikwama ka mlembi, konyamuliramo inki ndi zolembera. Anthuwo analowa mkati n’kuima pambali pa guwa lansembe lamkuwa.+
-