21 azim’bweretsa mtsikanayo pakhomo la nyumba ya bambo ake ndipo amuna a mumzindawo azim’ponya miyala kuti afe, chifukwa wachita chinthu chopusa ndi chochititsa manyazi mu Isiraeli,+ mwa kuchita uhule m’nyumba ya bambo ake.+ Motero muzichotsa woipayo pakati panu.+