-
2 Mbiri 15:8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Asa atangomva mawu amenewa ndi ulosi wa mneneri Odedi,+ analimba mtima n’kuyamba kuchotsa zinthu zonyansa+ m’dziko lonse la Yuda ndi Benjamini ndi m’mizinda imene analanda m’dera lamapiri la Efuraimu.+ Anayambanso kukonza guwa lansembe la Yehova limene linali patsogolo pa khonde la nyumba ya Yehova.+
-