20 “Ndakuchititsa kukhala ngati mpanda wamkuwa wolimba kwambiri kwa anthu awa.+ Iwo adzamenyana nawe ndithu, koma sadzakugonjetsa,+ pakuti ine ndili ndi iwe kuti ndikupulumutse ndi kukulanditsa,”+ watero Yehova.
8 Koma ine ndili ndi mphamvu zochuluka chifukwa cha mzimu wa Yehova. Ndine wokonzeka kuchita zachilungamo ndi kusonyeza mphamvu+ kuti ndiuze mbadwa za Yakobo za kupanduka kwawo, komanso kuti ndiuze Isiraeli za tchimo lake.+