Yesaya 47:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Alangizi ako ambirimbiri akutopetsa. Anthu opembedza zinthu zakumwamba, oyang’anitsitsa kayendedwe ka nyenyezi,+ amene amalosera zimene zichitike kwa iwe mwezi watsopano ukakhala, tsopano aimirire ndi kukupulumutsa. Danieli 5:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Pa nthawi imeneyo amuna onse anzeru anabwera kwa mfumu koma sanathe kuwerenga mawu olembedwawo kapena kuiuza mfumu kumasulira kwake.+ Danieli 5:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Tsopano ineyo anandibweretsera amuna anzeru ndi anthu okhulupirira mizimu kuti awerenge zolembedwazi ndi kundiuza kumasulira kwake, koma iwo alephera kumasulira mawuwa.+
13 Alangizi ako ambirimbiri akutopetsa. Anthu opembedza zinthu zakumwamba, oyang’anitsitsa kayendedwe ka nyenyezi,+ amene amalosera zimene zichitike kwa iwe mwezi watsopano ukakhala, tsopano aimirire ndi kukupulumutsa.
8 Pa nthawi imeneyo amuna onse anzeru anabwera kwa mfumu koma sanathe kuwerenga mawu olembedwawo kapena kuiuza mfumu kumasulira kwake.+
15 Tsopano ineyo anandibweretsera amuna anzeru ndi anthu okhulupirira mizimu kuti awerenge zolembedwazi ndi kundiuza kumasulira kwake, koma iwo alephera kumasulira mawuwa.+