12 Masamba ake anali okongola ndipo unali ndi zipatso zambiri. Mumtengomo munali zakudya zokwanira chamoyo chilichonse. Nyama zakutchire+ zinali kukhala mumthunzi wake.+ Mbalame zam’mlengalenga zinali kukhala panthambi zake+ ndipo zamoyo zonse zinali kupeza chakudya mmenemo.