64 “Yehova adzakumwazani mwa anthu a mitundu yonse kuchokera kumalekezero ena a dziko mpaka kumalekezero enanso a dziko.+ Kumeneko mukatumikira milungu ina imene inuyo kapena makolo anu simunaidziwe, milungu yamtengo ndi milungu yamwala.+
9 Pakuti taonani, ine ndalamula kuti nyumba ya Isiraeli igwedezedwe pakati pa mitundu yonse,+ monga mmene munthu amachitira posefa, ndipo mwala sudzadutsa kuti ugwere pansi.