17 Pakuti ndi Yehova Mulungu wathu amene anatitulutsa m’dziko la Iguputo+ pamodzi ndi makolo athu, kutichotsa m’nyumba yaukapolo.+ Iye anachita zizindikiro zazikulu pamaso pathu+ ndi kutiteteza m’njira yonse imene tinayenda, ndiponso kwa mitundu yonse ya anthu amene tinadutsa pakati pawo.+
8 “Yakobo atangofika mu Iguputo,+ makolo anu n’kuyamba kupempha thandizo+ kwa Yehova, Yehova anatumiza Mose+ ndi Aroni kuti atsogolere makolo anu potuluka mu Iguputo, ndipo anawapatsa dziko lino kuti akhalemo.+