4 Zinthu zimene mbozi zinasiya zinadyedwa ndi dzombe.+ Zimene dzombelo linasiya zinadyedwa ndi ana a dzombe oyenda pansi opanda mapiko ndipo zimene ana a dzombe oyenda pansiwo anasiya zinadyedwa ndi mphemvu.+
9 “‘Ndinawononga mbewu zanu ndi mphepo yotentha komanso ndi matenda a chuku.+ Munachulukitsa minda yanu ya mpesa ndi ya mbewu zina ndipo mbozi zinawononga mitengo yanu ya mkuyu ndi ya maolivi,+ komabe inu simunabwerere kwa ine,’+ watero Yehova.