Ekisodo 10:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Dzombelo linakuta nthaka yonse ya m’dzikolo+ ndipo dziko linachita mdima.+ Dzombelo linadya zomera zonse za m’dzikolo ndi zipatso zonse za m’mitengo zimene sizinawonongeke ndi matalala,+ moti sipanatsale chobiriwira chilichonse m’mitengo kapena pa zomera m’dziko lonse la Iguputo.+ Deuteronomo 28:38 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 38 “Udzapita ndi mbewu zambiri kumunda, koma udzakolola zochepa+ chifukwa dzombe lidzadya mbewuzo.+ Amosi 4:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 “‘Ndinawononga mbewu zanu ndi mphepo yotentha komanso ndi matenda a chuku.+ Munachulukitsa minda yanu ya mpesa ndi ya mbewu zina ndipo mbozi zinawononga mitengo yanu ya mkuyu ndi ya maolivi,+ komabe inu simunabwerere kwa ine,’+ watero Yehova.
15 Dzombelo linakuta nthaka yonse ya m’dzikolo+ ndipo dziko linachita mdima.+ Dzombelo linadya zomera zonse za m’dzikolo ndi zipatso zonse za m’mitengo zimene sizinawonongeke ndi matalala,+ moti sipanatsale chobiriwira chilichonse m’mitengo kapena pa zomera m’dziko lonse la Iguputo.+
9 “‘Ndinawononga mbewu zanu ndi mphepo yotentha komanso ndi matenda a chuku.+ Munachulukitsa minda yanu ya mpesa ndi ya mbewu zina ndipo mbozi zinawononga mitengo yanu ya mkuyu ndi ya maolivi,+ komabe inu simunabwerere kwa ine,’+ watero Yehova.