Deuteronomo 28:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Yehova adzakulanga ndi chifuwa chachikulu,+ kuphwanya kwa thupi koopsa, kutupa, kutentha thupi kwambiri, lupanga,+ mphepo yotentha yowononga mbewu+ ndi matenda a mbewu.+ Zimenezi zidzakusautsa kufikira utawonongeka. 1 Mafumu 8:37 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 37 “M’dzikomo mukagwa njala,+ mliri,+ mphepo yotentha yowononga mbewu, matenda ambewu a chuku,+ dzombe,+ mphemvu,+ komanso adani awo akawaukira m’zipata za mizinda yawo, ndiponso kukagwa mliri wamtundu uliwonse, nthenda yamtundu uliwonse, Hagai 2:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Anthu inu, ine ndinawononga mbewu zanu ndi mphepo yotentha,+ matenda a chuku+ ndi matalala.+ Zimenezi zinawononganso ntchito zonse za manja anu.+ Koma panalibe aliyense wa inu amene anabwerera kwa ine,’+ watero Yehova.
22 Yehova adzakulanga ndi chifuwa chachikulu,+ kuphwanya kwa thupi koopsa, kutupa, kutentha thupi kwambiri, lupanga,+ mphepo yotentha yowononga mbewu+ ndi matenda a mbewu.+ Zimenezi zidzakusautsa kufikira utawonongeka.
37 “M’dzikomo mukagwa njala,+ mliri,+ mphepo yotentha yowononga mbewu, matenda ambewu a chuku,+ dzombe,+ mphemvu,+ komanso adani awo akawaukira m’zipata za mizinda yawo, ndiponso kukagwa mliri wamtundu uliwonse, nthenda yamtundu uliwonse,
17 Anthu inu, ine ndinawononga mbewu zanu ndi mphepo yotentha,+ matenda a chuku+ ndi matalala.+ Zimenezi zinawononganso ntchito zonse za manja anu.+ Koma panalibe aliyense wa inu amene anabwerera kwa ine,’+ watero Yehova.