-
Yesaya 2:4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Mulungu adzakhala woweruza pakati pa mitundu+ ndipo adzakonza zinthu+ zokhudza mitundu yambiri ya anthu.+ Iwo adzasula malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo, ndi mikondo yawo kuti ikhale zida zosadzira mitengo.+ Mtundu wa anthu sudzanyamula lupanga kuti umenyane ndi mtundu unzake, ndipo anthuwo sadzaphunziranso nkhondo.+
-
-
Mika 4:3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Mulungu adzakhala woweruza pakati pa mitundu yambiri ya anthu+ ndipo adzakonza zinthu+ zokhudza anthu ochokera m’mitundu yamphamvu yakutali.+ Iwo adzasula malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo, ndi mikondo yawo kuti ikhale zida zosadzira mitengo.+ Mtundu wa anthu sudzanyamula lupanga kuti umenyane ndi mtundu unzake, ndipo anthuwo sadzaphunziranso nkhondo.+
-