-
2 Mbiri 7:6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Ansembe+ anali ataimirira m’malo awo a ntchito pamodzi ndi Alevi,+ onse atanyamula zipangizo zoimbira+ Yehova nyimbo zimene Davide+ mfumu anapanga kuti aziyamikira Yehova. Aleviwo anali kunena kuti “pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhala mpaka kalekale.” Iwo ankanena zimenezi paliponse pamene Davide akanatamanda Mulungu kudzera mwa iwo. Ansembe anali kuimba malipenga+ mokweza patsogolo pawo, Aisiraeli onse ataimirira.
-
-
2 Mbiri 29:25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Pa nthawi imeneyi, Hezekiya anaika Alevi+ panyumba ya Yehova atanyamula zinganga,+ zoimbira za zingwe,+ ndi azeze.+ Iwo anali kutsatira ndondomeko yoimbira imene anaikhazikitsa Davide,+ Gadi+ yemwe anali wamasomphenya wa mfumu, ndi mneneri Natani,+ popeza ndondomekoyo inachokera kwa Yehova kudzera mwa aneneri ake.+
-