6 Ana onsewa anali kuyang’aniridwa ndi bambo awo poimba nyimbo m’nyumba ya Yehova. Ankaimba nyimbozo ndi zinganga,+ zoimbira za zingwe,+ ndi azeze,+ pochita utumiki wa panyumba ya Mulungu woona.
Koma Asafu, Yedutuni, ndi Hemani anali kuyang’aniridwa ndi mfumu.+