6 M’chaka cha 9 cha Hoshiya, mfumu ya Asuri inalanda Samariya+ n’kutenga Aisiraeli kupita nawo ku Asuri.+ Mfumuyo inakaika Aisiraeliwo ku Hala+ ndi ku Habori pafupi ndi mtsinje wa Gozani,+ ndiponso m’mizinda ya Amedi.+
17 Yehova adzabweretsera iweyo,+ anthu ako, ndi nyumba ya bambo ako masiku amene sanakhaleponso kuyambira tsiku limene Efuraimu anapatukana ndi Yuda.+ Iye adzakubweretserani mfumu ya Asuri.+