Salimo 103:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 Yehova wakhazikitsa mpando wake wachifumu kumwamba.+Ndipo ufumu wake ukulamulira chilichonse.+ Salimo 115:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Kunena za kumwamba, kumwamba ndi kwa Yehova,+Koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.+ Salimo 136:26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 Yamikani Mulungu wakumwamba:+Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+