Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 1:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Komanso, Mulungu anawadalitsa+ n’kuwauza kuti: “Muberekane,+ muchuluke, mudzaze dziko lapansi, ndipo muliyang’anire.+ Muyang’anirenso+ nsomba zam’nyanja ndi zolengedwa zouluka m’mlengalenga, komanso cholengedwa chilichonse chokwawa padziko lapansi.”

  • Deuteronomo 32:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  8 Pamene Wam’mwambamwamba anapereka cholowa kwa mitundu,+

      Pamene analekanitsa ana a Adamu,+

      Anaika malire a anthu+

      Poganizira chiwerengero cha ana a Isiraeli.+

  • Salimo 37:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Olungama adzalandira dziko lapansi,+

      Ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.+

  • Yesaya 45:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Pakuti Yehova, Mlengi wa kumwamba,+ Mulungu woona,+ amene anaumba dziko lapansi ndi kulipanga,+ amene analikhazikitsa mwamphamvu,+ amene sanalilenge popanda cholinga, amene analiumba kuti anthu akhalemo,+ wanena kuti: “Ine ndine Yehova ndipo palibenso wina.+

  • Yeremiya 27:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 ‘Ine ndinapanga dziko lapansi,+ anthu+ ndi nyama+ zapadziko lapansi pogwiritsa ntchito mphamvu zanga zazikulu+ ndiponso dzanja langa lotambasula.+ Ndipo dzikoli ndalipereka kwa amene ndikufuna.+

  • Machitidwe 17:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Ndipo kuchokera mwa munthu mmodzi+ anapanga mtundu wonse wa anthu,+ kuti akhale padziko lonse lapansi.+ Iye anakhazikitsa nthawi zoikidwiratu+ komanso anaika malire achikhalire a malo oti anthu azikhala.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena