Masalimo
136 Yamikani Yehova anthu inu, pakuti iye ndi wabwino:+
Kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+
2 Yamikani Mulungu wa milungu:+
Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+

4 Yamikani Wochita zodabwitsa ndiponso ntchito zazikulu:+
Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+
5 Yamikani amene anapanga kumwamba mwanzeru:+
Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+
6 Yamikani woyala dziko lapansi pamwamba pa madzi:+
Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+
7 Yamikani wopanga zounikira zazikulu:+
Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+
8 Amenenso anapanga dzuwa kuti lizilamulira masana:+
Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+
9 Amene anapanga mwezi ndi nyenyezi kuti zizilamulira pamodzi usiku:+
Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+
10 Yamikani amene anakantha Aiguputo mwa kupha ana awo oyamba kubadwa:+
Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+
11 Yamikani amene anatulutsa Aisiraeli pakati pawo:+
Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+
12 Anawatulutsa ndi dzanja lamphamvu ndi mkono wotambasula:+
Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.
13 Yamikani amene anagawa pakati Nyanja Yofiira:+
Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+
14 Amenenso anachititsa Isiraeli kudutsa pakati pake:+
Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+
15 Amenenso anakutumulira Farao ndi gulu lake lankhondo m’Nyanja Yofiira:+
Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+
16 Yamikani amene anayendetsa anthu ake m’chipululu:+
Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+
17 Yamikani amene anapha mafumu amphamvu:+
Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+
18 Amenenso anapha mafumu olemekezeka:+
Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+
19 Iye anapha Sihoni mfumu ya Aamori:+
Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+
20 Anaphanso Ogi mfumu ya Basana:+
Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+
21 Ndipo dziko lawo analipereka kwa anthu ake kukhala cholowa:+
Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+
22 Cholowa cha Isiraeli mtumiki wake:+
Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+
23 Iye amene anatikumbukira pamene adani anatinyazitsa:+
Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+
24 Amene anatipulumutsa mobwerezabwereza kuchokera m’manja mwa adani athu:+
Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+
25 Amenenso amapereka chakudya kwa zamoyo zonse:+
Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+
26 Yamikani Mulungu wakumwamba:+