4 Apa n’kuti atagonjetsa Sihoni+ mfumu ya Aamori imene inali kukhala ku Hesiboni. Anali atagonjetsanso Ogi+ mfumu ya Basana imene inali kukhala ku Asitaroti.+ Mfumu imeneyi anaigonjetsera ku Edirei.+
10 Tinamva za mmene Yehova anaphwetsera madzi a Nyanja Yofiira pamaso panu, mutatuluka m’dziko la Iguputo.+ Tinamvanso za mmene munaphera+ mafumu awiri a Aamori, Sihoni+ ndi Ogi,+ kutsidya kwa Yorodano.
21 Pamenepo Yehova Mulungu wa Aisiraeli anapereka Sihoni ndi anthu ake onse m’manja mwa Aisiraeli. Choncho anawagonjetsa ndi kutenga dziko lonse la Aamori okhala kumeneko.+