Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 13:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Chotero Mulungu anachititsa ana a Isiraeli kuyenda njira yaitali yodutsa m’chipululu chapafupi ndi Nyanja Yofiira.+ Koma iwo potuluka m’dziko la Iguputo, anayenda mwa dongosolo lomenyera nkhondo.+

  • Ekisodo 15:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Kenako Mose anauza Isiraeli kuti anyamuke pa Nyanja Yofiira ndipo analowa m’chipululu cha Shura.+ Iwo anayenda m’chipululumo kwa masiku atatu, koma sanapeze madzi.+

  • Deuteronomo 8:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Muzikumbukira njira yonse imene Yehova Mulungu wanu anakuyendetsani m’chipululu zaka 40 zonsezi.+ Iye anakuyendetsani m’chipululu kuti akuphunzitseni kudzichepetsa,+ kukuyesani+ pofuna kudziwa zimene zinali mumtima mwanu,+ kuti aone ngati mukanasunga malamulo ake kapena ayi.

  • Deuteronomo 8:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Mungaiwale amene anakuyendetsani m’chipululu chachikulu ndi chochititsa mantha,+ chokhala ndi njoka zapoizoni,+ zinkhanira ndiponso dziko louma lopanda madzi. Amenenso anakutulutsirani madzi pamwala wolimba ngati nsangalabwi.+

  • Nehemiya 9:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Usana munali kuwatsogolera ndi mtambo woima njo ngati chipilala,+ ndipo usiku munali kuwatsogolera ndi moto woima njo ngati chipilala+ kuti uziwaunikira+ njira imene anayenera kuyendamo.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena