20 “Yehova adzakutumizira matemberero,+ chisokonezo+ ndi chilango+ pa ntchito zako zonse zimene ukuyesa kugwira. Adzakuchitira zimenezi kufikira utafafanizidwa ndi kutha mofulumira, chifukwa cha kuipa kwa zochita zako popeza kuti wandisiya.+
11 Alimi achita manyazi+ chifukwa cha tirigu ndi barele ndipo osamalira minda ya mpesa akulira mofuula. Zili choncho chifukwa chakuti zokolola za m’munda zawonongeka.+