Levitiko 19:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 “‘Usabwezere choipa+ kapena kusungira chakukhosi anthu amtundu wako.+ Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.+ Ine ndine Yehova. Maliko 12:31 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 31 Lachiwiri ndi ili, ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’+ Kulibe lamulo lina lalikulu kuposa amenewa.” Luka 10:27 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 27 Iye anayankha kuti: “‘Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, mphamvu zako zonse, ndi maganizo ako onse.’+ Komanso, ‘uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’”+ Akolose 3:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Koma kuwonjezera pa zonsezi, valani chikondi,+ pakuti chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu+ kwambiri kuposa chinthu china chilichonse. Yakobo 2:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Tsopano ngati inu mukutsatira lamulo lachifumu+ lakuti: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha,”+ monga mmene lemba limanenera, mukuchita bwino ndithu. 1 Petulo 1:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Tsopano, popeza mwayeretsa+ miyoyo yanu mwa kukhala omvera choonadi ndipo zotsatira zake n’zakuti mumakonda abale mopanda chinyengo,+ kondanani kwambiri kuchokera mumtima.+
18 “‘Usabwezere choipa+ kapena kusungira chakukhosi anthu amtundu wako.+ Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.+ Ine ndine Yehova.
31 Lachiwiri ndi ili, ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’+ Kulibe lamulo lina lalikulu kuposa amenewa.”
27 Iye anayankha kuti: “‘Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, mphamvu zako zonse, ndi maganizo ako onse.’+ Komanso, ‘uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’”+
14 Koma kuwonjezera pa zonsezi, valani chikondi,+ pakuti chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu+ kwambiri kuposa chinthu china chilichonse.
8 Tsopano ngati inu mukutsatira lamulo lachifumu+ lakuti: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha,”+ monga mmene lemba limanenera, mukuchita bwino ndithu.
22 Tsopano, popeza mwayeretsa+ miyoyo yanu mwa kukhala omvera choonadi ndipo zotsatira zake n’zakuti mumakonda abale mopanda chinyengo,+ kondanani kwambiri kuchokera mumtima.+