Salimo 41:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Koma munthu amene ndinali kukhala naye mwamtendere, amene ndinali kumukhulupirira,+Munthu amene anali kudya chakudya changa,+ wakweza chidendene chake kundiukira.+ Maliko 14:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Iye anati: “Ndi mmodzi wa inu 12, amene akusunsa nane m’mbale imodzi.+ Luka 22:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 “Koma taonani! Wondipereka+ ndili naye limodzi patebulo pompano.+ Yohane 13:26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 Yesu anayankha kuti: “Ndi amene ndimupatse chidutswa cha mkate chimene ndisunse.”+ Choncho atasunsa chidutswa cha mkate chija, anapatsa Yudasi, mwana wa Simoni Isikariyoti.
9 Koma munthu amene ndinali kukhala naye mwamtendere, amene ndinali kumukhulupirira,+Munthu amene anali kudya chakudya changa,+ wakweza chidendene chake kundiukira.+
26 Yesu anayankha kuti: “Ndi amene ndimupatse chidutswa cha mkate chimene ndisunse.”+ Choncho atasunsa chidutswa cha mkate chija, anapatsa Yudasi, mwana wa Simoni Isikariyoti.