Luka 6:47 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 47 Aliyense wobwera kwa ine kudzamva mawu anga, ndi kuwachita, ndikuuzani amene amafanana naye:+ Luka 6:48 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 48 Iyeyo ali ngati munthu womanga nyumba, amene anakumba mozama kwambiri ndi kuyala maziko pathanthwe. Ndipo pamene mtsinje unasefukira,+ madzi anawomba nyumbayo, koma sanathe kuigwedeza, chifukwa anaimanga bwino.+ Yakobo 1:25 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 25 Koma woyang’anitsitsa m’lamulo langwiro+ limene limabweretsa ufulu, amene amalimbikira kutero, adzakhala wosangalala+ polichita chifukwa chakuti sali wongomva n’kuiwala, koma wochita.+
48 Iyeyo ali ngati munthu womanga nyumba, amene anakumba mozama kwambiri ndi kuyala maziko pathanthwe. Ndipo pamene mtsinje unasefukira,+ madzi anawomba nyumbayo, koma sanathe kuigwedeza, chifukwa anaimanga bwino.+
25 Koma woyang’anitsitsa m’lamulo langwiro+ limene limabweretsa ufulu, amene amalimbikira kutero, adzakhala wosangalala+ polichita chifukwa chakuti sali wongomva n’kuiwala, koma wochita.+