45 Munthu wabwino amatulutsa zabwino m’chuma chabwino+ cha mtima wake. Koma munthu woipa amatulutsa zoipa m’chuma chake choipa, pakuti pakamwa pamalankhula zosefukira mumtima.+
6 Lilimenso ndi moto.+ Mwa ziwalo zathu zonse, lilime ndilo lili lodzaza ndi zosalungama chifukwa limadetsa thupi lonse.+ Lili ndi moto wa Gehena* ndipo limayatsa moyo wonse wa munthu.