Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Mbiri 20:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Anthuwo ananyamuka m’mawa kwambiri n’kupita kuchipululu+ cha Tekowa.+ Ali m’njira, Yehosafati anaimirira n’kunena kuti: “Tamverani inu Ayuda ndi anthu okhala mu Yerusalemu!+ Khulupirirani+ Yehova Mulungu wanu kuti mukhalitse. Khulupirirani aneneri+ ake kuti zinthu zikuyendereni bwino.”

  • Mateyu 17:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Iye anawayankha kuti: “Chifukwa cha kuchepa kwa chikhulupiriro chanu. Pakuti ndithu ndikukuuzani, ngati mutakhala ndi chikhulupiriro chofanana ndi kanjere ka mpiru kuchepa kwake, mudzatha kuuza phiri ili kuti, ‘Choka pano upite apo,’ ndipo lidzachokadi. Palibe chimene chidzakhala chosatheka kwa inu.”+

  • Maliko 11:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Ndithu ndikukuuzani kuti aliyense wouza phiri ili kuti, ‘Nyamuka pano udziponye m’nyanja,’ ndipo sakukayika mumtima mwake, koma ali ndi chikhulupiriro kuti zimene wanena zichitikadi, zidzaterodi.+

  • Luka 17:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Pamenepo Ambuye anawayankha kuti: “Mukanakhala ndi chikhulupiriro chofanana ndi kanjere ka mpiru kuchepa kwake, mukanatha kuuza mtengo wa mabulosi uwu kuti, ‘Zuka pano, kadzibzale m’nyanjamo!’ ndipo ukanakumverani.+

  • Yohane 11:40
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 40 Yesu anati: “Kodi sindinakuuze kuti ngati ukhulupirira udzaona ulemerero wa Mulungu?”+

  • Machitidwe 14:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Mwamuna ameneyu anali kumvetsera pamene Paulo anali kulankhula. Ndiyeno Paulo atamuyang’anitsitsa anaona kuti ali ndi chikhulupiriro+ ndipo angathe kuchiritsidwa.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena