23 Iye anawauza kuti: “Inde mudzamwadi+ zimene ndatsala pang’ono kumwa. Koma kunena zokhala kudzanja langa lamanja ndi lamanzere, si ine wopereka mwayi umenewo, koma Atate wanga adzaupereka kwa amene anawakonzera.”+
9 Ine Yohane, m’bale wanu ndi wogawana nanu masautso+ a Yesu,+ mu ufumu+ ndi m’kupirira,+ ndinali pachilumba cha Patimo chifukwa cholankhula za Mulungu ndi kuchitira umboni za Yesu.+