2 Kenako mngelo wa Yehova anaonekera kwa iye pakati pa chitsamba chaminga+ chimene chinali kuyaka moto. Atachiyang’anitsitsa, anaona kuti chitsamba chamingacho chikuyaka, koma sichikupsa.
37 Koma zakuti akufa amaukitsidwa ngakhalenso Mose anafotokoza m’nkhani ya chitsamba cha minga.+ M’nkhani imeneyo iye ananena kuti Yehova ndi ‘Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo.’+