6 Iye ananenanso kuti: “Ndine Mulungu wa atate ako, Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo.”+ Pamenepo Mose anaphimba nkhope yake, chifukwa anaopa kuyang’ana Mulungu woona.
3 Ndinali kuonekera kwa Abulahamu,+ Isaki+ ndi Yakobo+ monga Mulungu Wamphamvuyonse.+ Koma za dzina langa lakuti Yehova,+ ine sindinadzidziwikitse+ kwa iwo.