Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 12:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 M’kupita kwa nthawi, anasamuka pamalopo n’kupita kudera lamapiri, kum’mawa kwa Beteli.+ Kumeneko iye anamanga hema wake. Beteli anali kumadzulo kwake ndipo Ai+ anali kum’mawa kwake. Kenako anamangira Yehova guwa lansembe,+ n’kuyamba kuitana pa dzina la Yehova.+

  • Genesis 27:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Choncho anamuyandikira ndi kum’psompsona, ndipo anatha kumva kafungo ka zovala zake.+ Pamenepo anamudalitsa kuti:

      “Eya, kafungo ka mwana wanga kakununkhira ngati fungo lokoma la munda umene Yehova waudalitsa.

  • Genesis 28:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Kenako Yakobo anagalamuka ku tulo take n’kunena kuti: “Ndithudi Yehova ali pamalo pano, koma ine sindinadziwe.”

  • 2 Samueli 7:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Ndi mtundu uti padziko lapansi umene ungafanane ndi mtundu wa anthu anu Aisiraeli,+ amene inu Mulungu munawawombola monga anthu anu+ ndi kudzipangira dzina,+ amene munawachitira zinthu zazikulu ndi zochititsa mantha?+ Munapitikitsa mitundu ina ndi milungu yawo, chifukwa cha anthu anu amene munawawombola+ nokha kuchokera ku Iguputo.

  • Salimo 9:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Yehova amadziwika ndi ziweruzo zimene amapereka.+

      Woipa wakodwa mumsampha wa ntchito ya manja ake.+

      Higayoni.* [Seʹlah.]

  • Yesaya 52:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 “Pa chifukwa chimenecho anthu anga adzadziwa dzina langa.+ Adzalidziwa pa chifukwa chimenecho m’tsiku limenelo, pakuti ineyo ndi amene ndikulankhula.+ Ndithu ndineyo.”

  • Yeremiya 16:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 “Choncho ine ndiwaphunzitsa. Pa nthawi ino yokha ndiwaonetsa dzanja langa ndi mphamvu zanga,+ ndipo adziwa kuti dzina langa ndine Yehova.”+

  • Yeremiya 32:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Inu munachita zizindikiro ndi zozizwitsa m’dziko la Iguputo. Zimene munachitazo zikudziwikabe mpaka pano mu Isiraeli ndiponso pakati pa anthu onse.+ Munachita zimenezo kuti mudzipangire dzina mofanana ndi zimene mukufuna kuchita posachedwapa.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena