-
Danieli 12:1Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 “Pa nthawi imeneyo Mikayeli,+ kalonga wamkulu+ amene waimirira+ kuti athandize anthu a mtundu wako, adzaimirira.+ Ndiyeno padzafika nthawi ya masautso imene sinakhalepo kuyambira pamene mtundu woyambirira wa anthu unakhalapo kufikira nthawi imeneyo.+ Pa nthawi imeneyo aliyense mwa anthu a mtundu wako amene dzina lake lidzakhala litalembedwa m’buku+ adzapulumuka.+
-
-
Yoweli 2:2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Limeneli ndi tsiku lamdima ndi lachisoni,+ tsiku lamitambo ndi lamdima wandiweyani. Tsikuli lili ngati mmene kuwala kwa m’bandakucha kumakhalira pamwamba pa mapiri.+
“Pali mtundu wa anthu ambiri ndiponso amphamvu.+ Palibe mtundu wina umene ungafanane nawo kuyambira nthawi yakale+ ndipo sipadzakhalanso wina wofanana nawo ku mibadwomibadwo.
-