Ezekieli 34:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 “Nkhosa zosochera ndidzazifunafuna,+ zomwazika ndidzazibweza. Yothyoka mwendo ndidzaimanga mwendo wothyokawo. Yodwala ndidzailimbitsa, koma yonenepa+ ndi yamphamvu ndidzaiwononga. Ndidzaipatsa chiweruzo monga chakudya chake.”+ Mateyu 9:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Choncho pitani mukaphunzire tanthauzo la mawu akuti, ‘Ndikufuna chifundo, osati nsembe.’+ Chifukwa ine sindinabwere kudzaitana anthu olungama, koma ochimwa.” Mateyu 10:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 M’malomwake, nthawi zonse muzipita kwa nkhosa zosochera za nyumba ya Isiraeli.+ Luka 15:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 “Ndani wa inu amene atakhala ndi nkhosa 100, imodzi n’kutayika, sangasiye nkhosa 99 zinazo m’chipululu, n’kupita kukafunafuna imodzi yotayikayo kufikira ataipeza?+ Aroma 5:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Koma Mulungu akuonetsa chikondi chake+ kwa ife, moti pamene tinali ochimwa, Khristu anatifera.+ 1 Timoteyo 1:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Mawu akuti Khristu Yesu anabwera m’dziko kudzapulumutsa ochimwa,+ ndi mawu oona ndi oyenera kuwavomereza ndi mtima wonse.+ Mwa ochimwa amenewa, ine ndiye wochimwa kwambiri.+
16 “Nkhosa zosochera ndidzazifunafuna,+ zomwazika ndidzazibweza. Yothyoka mwendo ndidzaimanga mwendo wothyokawo. Yodwala ndidzailimbitsa, koma yonenepa+ ndi yamphamvu ndidzaiwononga. Ndidzaipatsa chiweruzo monga chakudya chake.”+
13 Choncho pitani mukaphunzire tanthauzo la mawu akuti, ‘Ndikufuna chifundo, osati nsembe.’+ Chifukwa ine sindinabwere kudzaitana anthu olungama, koma ochimwa.”
4 “Ndani wa inu amene atakhala ndi nkhosa 100, imodzi n’kutayika, sangasiye nkhosa 99 zinazo m’chipululu, n’kupita kukafunafuna imodzi yotayikayo kufikira ataipeza?+
15 Mawu akuti Khristu Yesu anabwera m’dziko kudzapulumutsa ochimwa,+ ndi mawu oona ndi oyenera kuwavomereza ndi mtima wonse.+ Mwa ochimwa amenewa, ine ndiye wochimwa kwambiri.+