3 Uzani khamu lonse la Isiraeli kuti, ‘Pa tsiku la 10 la mwezi uno mabanja onse ochokera mwa kholo limodzi atenge nkhosa imodziimodzi,+ banja lililonse litenge nkhosa imodzi.
13Tsopano Yesu anadziwiratu chikondwerero cha pasika chisanafike, kuti nthawi yake yochoka m’dzikoli kupita kwa Atate+ yakwana.+ Ndipo popeza kuti anali kuwakonda akewo amene anali m’dzikoli,+ anawakonda mpaka pa mapeto a moyo wake.