Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 18:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Ndidzawapatsa mneneri ngati iwe kuchokera pakati pa abale awo.+ Ndidzaika mawu anga m’kamwa mwake,+ ndipo adzawauza zonse zimene ndidzamulamula.+

  • Luka 7:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Zitatero anthu onse anagwidwa ndi mantha,+ moti anayamba kutamanda Mulungu, kuti: “Mneneri wamkulu+ waonekera pakati pathu.” Analinso kunena kuti, “Mulungu wacheukira anthu ake.”+

  • Yohane 3:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Iyeyu anabwera kwa Yesu usiku+ ndi kumuuza kuti: “Rabi,+ tikudziwa kuti inu ndinu mphunzitsi+ wochokera kwa Mulungu,+ chifukwa munthu sangathe kuchita zizindikiro+ zimene inu mumachita ngati Mulungu sali naye.”+

  • Yohane 6:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Tsopano anthuwo ataona zizindikiro zimene anachitazo, anayamba kunena kuti: “Mosakayika uyu ndi mneneri+ uja amene anati adzabwera padziko.”

  • Machitidwe 2:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 “Amuna inu a mu Isiraeli, imvani mawu awa: Yesu Mnazareti,+ ndi munthu amene Mulungu anamuonetsera poyera kwa inu. Anatero mwa ntchito zamphamvu,+ mwa zodabwitsa komanso mwa zizindikiro, zimene Mulungu anachita pakati panu kudzera mwa iye,+ monga mmene inunso mukudziwira.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena