13 Mulungu wa Abulahamu, wa Isaki ndi wa Yakobo,+ Mulungu wa makolo athu, ndi amene walemekeza+ Mtumiki+ wake Yesu, amene inu munamupereka+ ndi kumukana pamaso pa Pilato, Pilatoyo akufuna kumumasula.+
27 Pakuti okhala mu Yerusalemu ndi olamulira awo sanamudziwe Iyeyu.+ Koma pochita ngati oweruza, anakwaniritsa zinthu zonenedwa ndi Aneneri,+ zimene zimawerengedwa mokweza Sabata lililonse.