Genesis 17:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 Pamenepo Mulungu anati: “Ndithu Sara mkazi wako adzakuberekera mwana wamwamuna ndipo dzina lake udzamutche Isaki.+ Ndidzakhazikitsa pangano ndi iye, limene lidzakhala mpaka kalekale kwa mbewu yake yobwera pambuyo pa iye.+ Mika 7:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Zonse zimene munanena kwa Yakobo zinali zoona ndipo Abulahamu munamusonyeza kukoma mtima kosatha. Ifenso mudzatichitira zomwezo chifukwa n’zimene munalonjeza makolo athu kalekale.+ Agalatiya 3:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Tsopano, malonjezo anaperekedwa kwa Abulahamu+ ndi kwa mbewu yake.+ Malemba sanena kuti: “Kwa mbewu zako,” ngati kuti mbewuzo n’zambiri, koma amanena za mbewu imodzi+ kuti: “Kwa mbewu yako,”+ amene ndi Khristu.+
19 Pamenepo Mulungu anati: “Ndithu Sara mkazi wako adzakuberekera mwana wamwamuna ndipo dzina lake udzamutche Isaki.+ Ndidzakhazikitsa pangano ndi iye, limene lidzakhala mpaka kalekale kwa mbewu yake yobwera pambuyo pa iye.+
20 Zonse zimene munanena kwa Yakobo zinali zoona ndipo Abulahamu munamusonyeza kukoma mtima kosatha. Ifenso mudzatichitira zomwezo chifukwa n’zimene munalonjeza makolo athu kalekale.+
16 Tsopano, malonjezo anaperekedwa kwa Abulahamu+ ndi kwa mbewu yake.+ Malemba sanena kuti: “Kwa mbewu zako,” ngati kuti mbewuzo n’zambiri, koma amanena za mbewu imodzi+ kuti: “Kwa mbewu yako,”+ amene ndi Khristu.+