4 Titafufuza tinapeza ophunzira ndi kukhala nawo kumeneko masiku 7. Koma mouziridwa ndi mzimu,+ iwo anauza Paulo mobwerezabwereza kuti asakaponde mu Yerusalemu.
11 Iye anafika kwa ife ndi kutenga lamba wa Paulo. Kenako anadzimanga mapazi ndi manja ndi kunena kuti: “Mzimu woyera wati, ‘Mwiniwake wa lambayu, Ayuda adzamumanga+ chonchi ku Yerusalemu ndi kumupereka+ m’manja mwa anthu a mitundu ina.’”