6 Tsopano Paulo ataona kuti ena mwa iwo anali Asaduki+ ndipo ena anali Afarisi, anafuula m’khotimo kuti: “Amuna inu, abale anga, ine ndine Mfarisi,+ mwana wa Afarisi. Pano ndikuweruzidwa+ chifukwa cha chiyembekezo cha kuuka+ kwa akufa.”
5 Ineyo ndinadulidwa pa tsiku la 8,+ ndine wa mtundu wa Isiraeli, wa fuko la Benjamini,+ Mheberi wobadwa kwa Aheberi.+ Kunena za chilamulo, ndine Mfarisi.+