46 Chotero Paulo ndi Baranaba analankhula molimba mtima kuti: “Kunali koyenera kuti inu mukhale oyamba kuuzidwa mawu a Mulungu.+ Koma popeza kuti mukuwatayira kumbali+ ndipo mukudziweruza nokha kukhala osayenera moyo wosatha, ifeyo tikutembenukira kwa anthu a mitundu ina.+