23 Munthu ameneyu, monga woperekedwa mwa kufuna kwa Mulungu ndi kudziwiratu kwake zam’tsogolo,+ ndi amene inu munamukhomerera pamtengo ndi kumupha kudzera mwa anthu osamvera malamulo.+
24 Iye ananyamula machimo athu+ m’thupi lake pamtengo,+ kuti tilekane ndi machimo+ n’kukhala amoyo m’chilungamo. Ndipo “munachiritsidwa ndi mabala ake.”+