4 Ndipo anandiuza kuti, ‘Ndidzakupatsa ana,+ ndipo mwa iwe mudzatuluka mitundu yambiri ya anthu.+ Dziko ili ndidzalipereka kwa mbewu yako kuti lidzakhale dziko lawo mpaka kalekale.’+
49 “Kwera m’phiri ili la Abarimu,+ phiri la Nebo,+ limene lili m’dziko la Mowabu, moyang’anana ndi Yeriko, ndipo uone dziko la Kanani limene ndikupereka kwa ana a Isiraeli kuti likhale lawo.+
24 Choncho ana awo+ analowa ndi kutenga dzikolo,+ ndipo munagonjetsa+ anthu okhala m’dzikolo, Akanani,+ ndi kuwapereka m’manja mwawo. Munaperekanso ngakhale mafumu a Akananiwo+ ndi mitundu ya anthu ya m’dzikolo+ kwa ana a Isiraeliwo kuti awachite zimene akufuna.+