Genesis 41:40 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 40 Iweyo ukhala woyang’anira nyumba yanga,+ ndipo anthu anga onse azimvera iweyo.+ Ine ndikhala wokuposa pa ufumu wokha.”+ Genesis 41:41 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 41 Farao anauzanso Yosefe kuti: “Tsopano ndikukuika kukhala woyang’anira dziko lonse la Iguputo.”+ Genesis 41:46 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 46 Yosefe anali ndi zaka 30+ pamene anayamba kutumikira Farao, mfumu ya Iguputo. Kenako anachoka pamaso pa Farao n’kuyamba kuyendera dziko lonse la Iguputo. Salimo 105:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Anamuika kukhala mkulu woyang’anira banja lake,+Komanso wolamulira chuma chake chonse.+
40 Iweyo ukhala woyang’anira nyumba yanga,+ ndipo anthu anga onse azimvera iweyo.+ Ine ndikhala wokuposa pa ufumu wokha.”+
46 Yosefe anali ndi zaka 30+ pamene anayamba kutumikira Farao, mfumu ya Iguputo. Kenako anachoka pamaso pa Farao n’kuyamba kuyendera dziko lonse la Iguputo.