11 Ndakhala wodzikweza tsopano. Ndinu mwandikakamiza+ kukhala wotero, popeza simunanene za zinthu zabwino zimene ndachita, ngakhale kuti munayenera kutero. Pakuti sindinachepe mwanjira ina iliyonse kwa atumwi anu apamwambawo,+ ngakhale kuti si ine kanthu m’maso mwanu.+
6 Tsopano kunena za anthu amene ankaoneka ngati apadera,+ kaya pa chiyambi anali anthu otani, zilibe kanthu kwa ine,+ Mulungu sayang’ana nkhope ya munthu,+ kwa ine, amuna odalirika amenewo sanandiphunzitse kalikonse katsopano.