Aroma 3:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Chotero pamaso pake palibe munthu amene adzayesedwe wolungama+ mwa ntchito za chilamulo,+ popeza chilamulo chimachititsa kuti tidziwe uchimo molondola.+ Aroma 4:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Kwenikweni, Chilamulo chimabala mkwiyo,+ koma pamene palibe lamulo, palibenso kulakwa.+ Aroma 7:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Choncho, Chilamulo kumbali yake n’choyera,+ ndipo malamulo ndi oyera, olungama+ ndi abwino.+ Aroma 7:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Pakuti tikudziwa kuti Chilamulo n’chauzimu,+ koma ine ndine wakuthupi, wogulitsidwa ku uchimo.+
20 Chotero pamaso pake palibe munthu amene adzayesedwe wolungama+ mwa ntchito za chilamulo,+ popeza chilamulo chimachititsa kuti tidziwe uchimo molondola.+