Miyambo 15:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Kuyankha modekha kumabweza mkwiyo,+ koma mawu opweteka amayambitsa mkwiyo.+ 1 Akorinto 4:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Kodi mukufuna chiyani? Mukufuna ndibwere kwa inu ndi chikwapu,+ kapena ndi chikondi ndi mzimu wofatsa?+ Akolose 3:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Chotero monga ochita kusankhidwa ndi Mulungu,+ oyera ndi okondedwa, valani chifundo+ chachikulu, kukoma mtima, kudzichepetsa,+ kufatsa,+ ndi kuleza mtima.+ 1 Timoteyo 6:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Koma munthu wa Mulungu iwe, thawa zinthu zimenezi.+ M’malomwake tsatira chilungamo, kudzipereka kwa Mulungu, chikhulupiriro, chikondi, chipiriro, ndi kufatsa.+ Tito 3:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Asamanenere zoipa munthu aliyense, ndipo asakhale aukali.+ Koma akhale ololera,+ ndi ofatsa kwa anthu onse.+
21 Kodi mukufuna chiyani? Mukufuna ndibwere kwa inu ndi chikwapu,+ kapena ndi chikondi ndi mzimu wofatsa?+
12 Chotero monga ochita kusankhidwa ndi Mulungu,+ oyera ndi okondedwa, valani chifundo+ chachikulu, kukoma mtima, kudzichepetsa,+ kufatsa,+ ndi kuleza mtima.+
11 Koma munthu wa Mulungu iwe, thawa zinthu zimenezi.+ M’malomwake tsatira chilungamo, kudzipereka kwa Mulungu, chikhulupiriro, chikondi, chipiriro, ndi kufatsa.+
2 Asamanenere zoipa munthu aliyense, ndipo asakhale aukali.+ Koma akhale ololera,+ ndi ofatsa kwa anthu onse.+