Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 8:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Ndiyeno anauza Aroni ndi ana ake kuti: “Wiritsani+ nyamayo pakhomo la chihema chokumanako, ndipo muidyerenso pomwepo+ pamodzi ndi mkate umene uli m’dengu logwiritsidwa ntchito polonga anthu unsembe, monga mmene anandilamulira, kuti, ‘Aroni ndi ana ake adye zimenezi.’

  • Luka 10:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Choncho khalani m’nyumba yamtendereyo.+ Muzidya ndi kumwa zimene angakupatseni,+ chifukwa wantchito ayenera kulandira malipiro ake.+ Musamachoke kumene mwafikirako n’kupita kunyumba zina.+

  • Aroma 15:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Ndi zoona kuti achita zimenezo mwa kufuna kwawo, komabe iwo anali ndi ngongole kwa oyerawo. Pakuti ngati anthu a mitundu ina alandirako zinthu zauzimu+ kuchokera kwa oyerawo, ndiye kuti anthu a mitundu inawo ayeneranso kutumikira oyera amenewa mwa kuwapatsa zinthu zofunika pa moyo wawo wa tsiku ndi tsiku.+

  • 1 Akorinto 9:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Ngati tabzala zinthu zauzimu+ mwa inu, kodi ndi nkhani yaikulu ngati tikukolola zinthu zakuthupi mwa inu?+

  • Aheberi 13:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Komanso, musaiwale kuchita zabwino+ ndi kugawana zinthu ndi ena, pakuti nsembe zotero Mulungu amakondwera nazo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena