13 Timalankhulanso zinthu zimenezi, osati ndi mawu ophunzitsidwa ndi nzeru za anthu,+ koma ndi mawu amene mzimu+ watiphunzitsa, pamene tikuphatikiza zochitika zauzimu ndi mawu auzimu.+
16 Ndithudi, pamene ifeyo tinakudziwitsani za mphamvu ya Ambuye wathu Yesu Khristu ndi za kukhalapo* kwake,+ sitinatengere nkhani zabodza zopekedwa mochenjera ndi anthu,+ koma tinachita zimenezo chifukwa tinachita kuona ndi maso athu ulemerero wake.+