48 Aliyense wondinyalanyaza ndi kusalandira mawu anga, ali naye mmodzi womuweruza. Mawu+ amene ine ndalankhula ndi amene adzamuweruze pa tsiku lomaliza.
5 Chotero musaweruze+ kalikonse nthawi isanakwane, mpaka Ambuye adzafike.+ Akadzafika adzaunika zinsinsi za mu mdima+ ndi kuonetsa poyera+ zolingalira za m’mitima, ndipo aliyense adzatamandidwa yekha ndi Mulungu.+